CHIKHULUPILIRO NDI NTCHITO

Derek Prince
Published: 1970
Last Updated: நவம்பர் 2026
Read Time: 48
This teaching is not currently available in தமிழ்.
Kuyesera kupeza chilungamo kudzera mu malamulo kumabweretsa kunyada ndikusemphana ndi chisomo cha Mulungu. Derek Prince amatanthauzira kusiyana kwa chikhulupiriro chopulumutsa ndi ntchito, kuphunzitsa kuti okhulupirira amapangidwa mwa Khristu kuti achite ntchito zabwino atalandira chilungamo mwa chikhulupiriro.
Transcript
Ndipo usiku uno, kulengeza kwathu kukugwirizana mwachindunji ndi mutu womwe ndikhale ndikuyankhula. .Watengedwa kuchokera mu Aefeso 2:8–10
pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwachikhulupiriro ndipo ichi chosachokera kwwa inu: chiri mphatso ya Mulungu- chosachokera ku ntchitokuti asazitamandire munthu aliyense, pakuti ife ndife chipangano chake, olengedwa mwa khristu Yesu kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu kuti tikayende m'menemo.
Tsopano ndikupitiriza ndi mutu womwe ndidayamba nawo mu msonkhano wathu wapitawu; ndiye kuti, kuunika ziphunzitso zisanu ndi chimodzi zazikulu za chikhulupiriro cha Chikhristu zomwe zatchulidwa mu Ahebri 6:1 ndi 2. Ndikungobwereza mwachidule. Kulapa kuchokera ku ntchito zakufa, chikhulupiriro kwa Mulungu, chiphunzitso cha ubatizo, kuyika manja, kuuka kwa akufa ndi chiweruzo chamuyaya. Mu msonkhano wathu wapitawu ndinachita ndi mutu wakuti “Kudzera mu Kulapa kupita ku Chikhulupiriro.” Ndinachita ndi kulapa ndipo ndinayamba kuchita ndi chikhulupiriro. Ndikufuna kupitiriza usiku uno ndikuchita ndi chikhulupiriro ndipo mutuwo ndi “Chikhulupiriro ndi Ntchito,” mawu awiri osavuta omwe amagwiritsidwa ntchito kwambiri mu Chipangano Chatsopano ndipo komabe n’zochititsa chidwi kwambiri kuti anthu ambiri a Mulungu alibe kumvetsetsa bwino ubale pakati pa chikhulupiriro ndi ntchito.
Ndiloleni ndinene ndikuti mwa chikhulupiriro timatanthauza chabe zomwe timakhulupirira, mwa ntchito timatanthauza chabe zomwe timachita. Kodi ubale wolondola pakati pa zomwe timakhulupirira ndi zomwe timachita ndi wotani?
Mwachidule ndikufuna ndifotokoze za Uthenga Wabwino. Ambiri mwaife timagwiritsa mau oti Uthenga wabwino' ndipo timayankhula za izo ngati ndichinthu china chake chome timachidziwa kwambiri zomwe tikutanthaudza. Zoona zake ndikuganiza kuti anthu ambiri amayankhula za uthenga wabwino pomwe sakudzindikira chomwe uthenga uli.Paulo akufotokoza mwa chindunji mu 1 Akorinto 15: 1-5
“Komanso, abale, ndikulengeza kwa inu uthenga wabwino umene ndinakuwuzani, umene munalandira komanso umene mukuyimirira. Koma umene umakupulumutsani ngati mutagwira mwamphamvu mawu amene ndinakuwuzani, pokhapokha ngati munakhulupirira pachabe.”
Ndipo Paulo amapita patsogolo kufotokoza uthenga wabwino. Uthenga wabwino umatchulidwa m’zochitika zitatu zosavuta za mbiri yakale, sizovuta.
Ndipo ndinakupatsani choyamba chimene ndinalandira, kuti Khristu anafa chifukwa cha machimo athu monga mwa Malemba, kuti anayikidwa m’manda ndi kuti anaukanso tsiku lachitatu, monga mwa Malemba.
Choncho uthenga wabwino umakhala ndi mfundo zitatu zosavuta zachikhalidwe: Khristu anafa chifukwa cha machimo athu, anayikidwa m'manda ndipo anaukitsidwa tsiku lachitatu. Ndipo pamene mawu amenewa sanatchulidwe, uthenga wabwino sukulalikidwa, pali kulalikira kwakukulu komwe kumatchedwa uthenga wabwino komwe sikuli ndi uthenga wabwino. Izi ndi mfundo zitatu zofunika zomwe tiyenera kuziganizira: Khristu anamwalira chifukwa cha machimo athu, anayikidwa m'manda ndipo anaukitsidwa tsiku lachitatu.
Ndipo mphamvu yoyesa yoyamba simboni zomwe zi ndipo mumalandira malipiro anu, si chisomo, ndi chinthu chimene chimakuyenererani. Koma iye akuti si momwe timapeza chilungamo. Si chifukwa cha ntchito zathu, si chinthu chimene tinalandira.
குறியீடு: MV-4163-100-NYA
