CHIKHULUPILIRO NDI NTCHITO

Derek Prince
Published: 1970
Last Updated: novembre 2026
Read Time: 48
This teaching is not currently available in Français.
Kuyesera kupeza chilungamo kudzera mu malamulo kumabweretsa kunyada ndikusemphana ndi chisomo cha Mulungu. Derek Prince amatanthauzira kusiyana kwa chikhulupiriro chopulumutsa ndi ntchito, kuphunzitsa kuti okhulupirira amapangidwa mwa Khristu kuti achite ntchito zabwino atalandira chilungamo mwa chikhulupiriro.
Transcript
Ndipo usiku uno, kulengeza kwathu kukugwirizana mwachindunji ndi mutu womwe ndikhale ndikuyankhula. .Watengedwa kuchokera mu Aefeso 2:8–10
pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwachikhulupiriro ndipo ichi chosachokera kwwa inu: chiri mphatso ya Mulungu- chosachokera ku ntchitokuti asazitamandire munthu aliyense, pakuti ife ndife chipangano chake, olengedwa mwa khristu Yesu kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu kuti tikayende m'menemo.
Tsopano ndikupitiriza ndi mutu womwe ndidayamba nawo mu msonkhano wathu wapitawu; ndiye kuti, kuunika ziphunzitso zisanu ndi chimodzi zazikulu za chikhulupiriro cha Chikhristu zomwe zatchulidwa mu Ahebri 6:1 ndi 2. Ndikungobwereza mwachidule. Kulapa kuchokera ku ntchito zakufa, chikhulupiriro kwa Mulungu, chiphunzitso cha ubatizo, kuyika manja, kuuka kwa akufa ndi chiweruzo chamuyaya. Mu msonkhano wathu wapitawu ndinachita ndi mutu wakuti “Kudzera mu Kulapa kupita ku Chikhulupiriro.” Ndinachita ndi kulapa ndipo ndinayamba kuchita ndi chikhulupiriro. Ndikufuna kupitiriza usiku uno ndikuchita ndi chikhulupiriro ndipo mutuwo ndi “Chikhulupiriro ndi Ntchito,” mawu awiri osavuta omwe amagwiritsidwa ntchito kwambiri mu Chipangano Chatsopano ndipo komabe n’zochititsa chidwi kwambiri kuti anthu ambiri a Mulungu alibe kumvetsetsa bwino ubale pakati pa chikhulupiriro ndi ntchito.
Ndiloleni ndinene ndikuti mwa chikhulupiriro timatanthauza chabe zomwe timakhulupirira, mwa ntchito timatanthauza chabe zomwe timachita. Kodi ubale wolondola pakati pa zomwe timakhulupirira ndi zomwe timachita ndi wotani?
Mwachidule ndikufuna ndifotokoze za Uthenga Wabwino. Ambiri mwaife timagwiritsa mau oti Uthenga wabwino' ndipo timayankhula za izo ngati ndichinthu china chake chome timachidziwa kwambiri zomwe tikutanthaudza. Zoona zake ndikuganiza kuti anthu ambiri amayankhula za uthenga wabwino pomwe sakudzindikira chomwe uthenga uli.Paulo akufotokoza mwa chindunji mu 1 Akorinto 15: 1-5
“Komanso, abale, ndikulengeza kwa inu uthenga wabwino umene ndinakuwuzani, umene munalandira komanso umene mukuyimirira. Koma umene umakupulumutsani ngati mutagwira mwamphamvu mawu amene ndinakuwuzani, pokhapokha ngati munakhulupirira pachabe.”
Ndipo Paulo amapita patsogolo kufotokoza uthenga wabwino. Uthenga wabwino umatchulidwa m’zochitika zitatu zosavuta za mbiri yakale, sizovuta.
Ndipo ndinakupatsani choyamba chimene ndinalandira, kuti Khristu anafa chifukwa cha machimo athu monga mwa Malemba, kuti anayikidwa m’manda ndi kuti anaukanso tsiku lachitatu, monga mwa Malemba.
Choncho uthenga wabwino umakhala ndi mfundo zitatu zosavuta zachikhalidwe: Khristu anafa chifukwa cha machimo athu, anayikidwa m'manda ndipo anaukitsidwa tsiku lachitatu. Ndipo pamene mawu amenewa sanatchulidwe, uthenga wabwino sukulalikidwa, pali kulalikira kwakukulu komwe kumatchedwa uthenga wabwino komwe sikuli ndi uthenga wabwino. Izi ndi mfundo zitatu zofunika zomwe tiyenera kuziganizira: Khristu anamwalira chifukwa cha machimo athu, anayikidwa m'manda ndipo anaukitsidwa tsiku lachitatu.
Ndipo mphamvu yoyesa yoyamba simboni zomwe zi ndipo mumalandira malipiro anu, si chisomo, ndi chinthu chimene chimakuyenererani. Koma iye akuti si momwe timapeza chilungamo. Si chifukwa cha ntchito zathu, si chinthu chimene tinalandira.
Tsopano, Paulo akupitiliza kufotokoza kuti ngati titalandira mfundo zosavuta izi mwa chikhulupiriro, popanda ntchito, popanda zomwe timachita, chilungamo chidzatipatsidwa. Tidzawerengedwa kukhala olungama. Ndikofunika kwambiri kuona kuti Paulo akuti si chifukwa cha zomwe timachita koma chifukwa cha zomwe timakhulupirira. Si chifukwa cha ntchito koma ndi chifukwa cha chikhulupiriro. Iye akupitiliza mu Aroma chaputala 4 kukambirana phunziro lomwe tingaphunzire kuchokera kwa Abrahamu chifukwa akuti Abrahamu anapatsidwa chilungamo chifukwa cha chikhulupiriro. Kenako Paulo amayamba kukambirana phunziro lomwe timaphunzira kuchokera pa izi. Iye akuti mu Aroma 4:
"Koma kwa iye amene amagwira ntchito, malipiro samawerengedwa ngati chisomo koma ngati ngongole."
Ngati mukugwira ntchito kwa wina ndipo mulandira malipiro anu, chimenecho si chisomo ndi chinthu chomwe muyenera kulandira. Koma iye akuti si momwe timapeza chilungamo. Sikuti ndi chifukwa cha ntchito zathu, si chinthu chomwe tinalandira.
akupitilidzabe ndi mau osangalatsa, ndipo ndikukuudzani kuti ngati simunadabwitsidwepo ndi zomwe mwawerenga mu Buku lopatulika ndithudi inu simunawerenge Buku lopatulika, chifukwa liri ndi mau ambiri odabwitsa. Paulo akupitiliza ku yankhula mu Aroma 4:5
“Koma kwa iye amene sachita ntchito koma amakhulupirira pa iye amene amayesa olakwa kukhala olungama, chikhulupiriro chake chimawerengedwa kukhala chilungamo.”
Choncho, ngati mukufuna kuti chikhulupiriro chanu chionekere kwa inu ngati chilungamo, chinthu choyamba chomwe muyenera kuchita ndi kusiya kugwira ntchito. "Kwa iye amene sagwira ntchito." Monga momwe mukuganizira kuti mungathe kupeza chilungamo mwa zomwe mukuchita, simudzachilandira. Ichi ndi chinthu chovuta kwambiri kwa anthu achipembedzo. Tazolowera lingaliro lakuti tiyenera kuchita chinachake kuti tipeze chisomo cha Mulungu. Chisomo sichingapezeke. Chisomo sichingapezeke. Mwa tanthauzo, sizingapezeke. Choncho, chinthu choyamba chomwe muyenera kuchita ngati mukufuna kuonedwa ngati olungama ndi Mulungu ndi kusiya kuyesa. Osagwira ntchito. Izi ndi zonena zodabwitsa kwa anthu ambiri koma ndiye kuti Baibulo ndi buku lodabwitsa. Zodabwitsa kwambiri kuposa momwe ambiri a ife timazindikira.
Kodi ubale oona weniweni pakati pa chikhulupiliro ndi ntchito nchiyani? Sikuti ntchito ndizosafunikira iyayi, ndidongosolo lomwe tidachokeramo. Rute ndi ine tinagwira mau apa Aefeso 2 omwe ndibwererekonso. Aefeso 2:8-10
“Pakuti ndi chisomo mwapulumutsidwa kudzera mu chikhulupiriro, ndipo ichi sichochokera kwa inu; ndi mphatso ya Mulungu…”
Sitikhoza kunyoza ngakhale kuti tinali ndi chikhulupiriro chifukwa tinangokhala ndi chikhulupiriro chifukwa Mulungu anatipatsa. Sio chinthu chomwe tingathe kupanga tokha.
Ndipo limanena kuti:
sichifukwa cha ntchito kuti yense angazitamandire
ndipo malo ambiri omwe amatchula anthu amene amakhulupirira kuti apangidwa olungama ndi ntchito zawo, Paulo akuti ayi, kuti asadzitamandire. Mukuona, chipembedzo cha ntchito chimakulitsa kunyada kwa munthu. Ndipo kunyada ndi tchimo lalikulu. Choncho, Mulungu wakonza njira yokhala olungama yomwe siikulitsa kunyada kwathu.
Ngati mungaganizire anthu omwe ali ndi zipembedzo zovuta kwambiri, ndipo sindikufuna kutchula chilichonse chifukwa sindikufuna kuoneka ngati ndikuwukira chilichonse, koma makamaka zipembedzo zikakhala zovuta kwambiri, amakhala onyada kwambiri. Akuchita zinthu zovuta kwambiri: kusala kudya, kupereka nsembe ndi zina zotero. Izi zimakulitsa kunyada. Mulungu amatsutsa onyada koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa. Choncho Mulungu wapanga njira yoti tikhale olungama naye yomwe siyikulitsa kunyada kwathu.
sindikudziwa kaya munazindikirapo koma tiyeni tikambe za akhrisitu. Akhrisitu omwe nga lamulo kwambiri, a khama ndi malamulo,anthu osakonda kwambiri kodi munaziona izi? Mukapita kwa iwo kufuna chikondi mutha osachipeza chokwanira. komabe, mwamalamulo ndi chikondi ndizo siyanirako pang'ono. ndiye tikuyenera kupitiliza kuziyang'anira mosamala kuchinthu chipembedzo nthawi zina chimayambitsa kuzikudza. ngati chili chipembedzo chopanda chisomo cha Mulungu chimayambitsa kuzikudza.
Koma pali malo antchito. sikuti siofunikira, pamangofunikira kuwaika mundondomeko.Aefeso 2:10 akufotokoza momveka monga zomwe ndimaziziwa.
Pakuti ndife ntchito yake, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zomwe Mulungu anakonza kale kuti tiziyenda m'menemo.
Choncho pamene Mulungu watilenga mwatsopano mwa Khristu, ndipo Buku lopatulika limanena kuti ngati wina ali mwa Khristu ndiye cholengedwa chatsopano, ndiye kuti Mulungu ali ndi ntchito zoyenera zokonzedwa kale kwa cholengedwa chatsopanocho. Koma chikhalidwe chakale cha thupi sichingathe kuyenda mu ntchito zabwino zomwe Mulungu wakonza. Muyenera kulengedwa mwatsopano mwa chikhulupiriro musanayambe kuyenda mu ntchito zabwino. Kenako ntchito zabwino zimakhala zofunika kwambiri. Koma muyenera kupeza dongosolo loyenera. Choyamba, cholengedwa chatsopano kudzera mu chikhulupiriro; kenako ntchito zabwino zomwe Mulungu wakonzeratu kale kwa ife.
Sindikudziwa ngati mwazindikira, simukuyenera kugwira ntchito pazimene mungamuchitire Mulungu, ngati mwakhala cholengedwa chatsopano mwa Khristu, n'chifukwa kuti Mulungu anazikonza kale izi. chomwe mungachite ndukufufza ntchito zomwe Mulungu anakonzeratu kwa inu musanabadwe. osayeserala kupanga ndondomeko zanu za moyo wanu, fufuzani chomwe ndondomeko ya Mulungu ili pa inu. Nthawi zambiri ndi zinthu zosiyana ndizimene timayembekedza.
Ndikupatseni chitsanzo mwachidule kuchokera kuzomwe ndadutsamo. Ndinali mwana modzi yekhayo, ndinalibe mchimwene kapena mlongo. Ndinakulira kusukulu yogonera konko kuyambira ndili ndi zaka 9 zakubadwa mpaka 25. kunali kondivuta kukumna ndi atsikana ngakhale ndinali nawo ochepa anzanga achitsikana. poyamba atsikana chinali chithu chodabwitsa chomwe sindimadziwa kuchedza nao. koma Mulungu atandi itana, ndinakwatira mkazi yemwe anali ndi nyumba yosungiramo ana ndipo tsiku lomwero ndinamukwatira ndinasanduka bambo wa ana 8 omwe ndinawapedza. Mukuona simukanaganiza kuti sichinali chinthu choyenera kwa Derek Prince. Ndikana ika ndondomeko za moyo wanga izi sizikanakhoza kukhala mbali imodzi. Koma zinali ntchito zabwino zomwe Mulungu anandikonzera kuti ndiyendemo. ndimakhutitsidwa, ngakhale ndimalephera nthawi zambiri, kuzindikira kuti choyamba ndayenda mu ntchito zabwino zomwe Mulungu anandikonzera ine.
Tsopano tibwere pang'ono ku tanthaudzo, apa ndipamene tikusowekera kuganiza mozama. Tikuyenera kuganiza modzama nthawi zonse! Ndiangati mukugwirizana nazo? chabwino tikuyenera kukambirana mwachidule za chikhalidwe cha chisomo. chisomo ndi mau okongola koma omwe nthawi zambiri sagwiritsidwa ntchito bwino. Ndimalalikira nthawi inayake mu mpingo wina ndipo ndinati,'kunena zoona mipingo yomwe imadzitcha chisomo' ndi mipingo yomwe imadziwa zochepa za chisomo'. Ndipo ndinadzuka ndi fundo yomwe ndimalalikira mu umodzi wa mipingo! komabe zikukhalabe zoona. Anthu ambiri omwe amagwiritsa ntchito mau oti chisomo alibe lingaliro lililonse zachomwe zikutanthaudza. Mudzu wa tathaudzo la chisomo ndi kukongola,.ndipo ndizokongola kuti Mulungu wayamba kuikidza mwa ife chifukwa timamukhulupirira iye. Amatipanga ife okongola ndi chisomo chake.
ndipo Paulo akunene mu Aroma 11:6
'Ngati chili chisomo, ndiye simwa ntchitoso. chifukwa ndiye chisomo sichikhalaso chisomo.
Munjira ina muchinenero changa sungalipidwe chisomo. chilichonse unga peze si chisomo. uku nthawi zambiri ndikudzichepetsa kwa anthu ambirife. timayenera kudalira pa chisomo chake,sitinga lipidwe chisomo.palibe chomwe tingachite kuti tipeze chisomo cha Mulungu. Ndipo pomwe ukusangalala kuti uli ndi chikhulupiliro, kumbukira Paulo akupitiliza kunena:
ndipo izo sizaife ndi mphatso ya Mulungu.
Mulibe chilichonse choti muzitamandire ngati mwapulumutsidwa mwa chikhulupiliro. Mulungu wachita izi kuti akutetezeni ku tchimo lalikulu lomwe ndi kuzikonda
Ndikuganizira ubale pakati pa chikhulupiliro ndi ntchito, zomwe timakhulupilira ndi zomwe timachita. Mene ndikudziwira ine, zonse zomwe ndingayankhule zitengedwa mu chipangano chatsopano koma kwa ambiri ainu zikhala zotutumutsa ngakhaleso kudabwitsa. Ndadzindikira izi kulalika chabe uthenga osavuta muchipangano chatsopano wa chipulumutso mwa chisomo ndi zotutumutsa kwa akhrisitu ambiri ongoyankhula.
Ndikukumbukira kuti ndinayankhulapo nthawi inayake pa chisisimuso zokhuza mulingo umenewu ngakhale kuti chikhrisitu si unyinji wa malamulo. Ndinawayang'ana anthu onse ndipo anazizimuka. Ndikuganiza kuti akanazizimuka pang'ono ndikanayankhula kuti, Mulungu wafa. kwa iwo maganizo awo anali oti chikhrisitu chinali unyinji lamalamulo. Mwina nanu muli maganizo ngati omwewo. Ndikufuna ndikuuzeni , chikhrisitu si unyinji wa malamulo: simungachipindule ndi malamulo
Kodi munthu angakhale bwanji wa chilungamo pamaso pa Mulungu?
Anzake achipembedzo onse ananyoza ganizo loti aliyense atha kukhala wa chilungamo pamaso pa Mulungu. Koma Mulungu anamva kulirako ndipo patadutsa zaka zambiri kudzera mukalata yaku Aroma anayankha funso 'Kodi munthu angakhake bwanji wa chilungamo pamaso pa Mulungu? Siposunga unyinji wa amalamulo.
Mu Aroma 3:20 Paulo akuti:
Chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayetsedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.
Tsopano ndaawerenga kutanthaudzira uku komwe kuli mu New King James. Mu NIV kwenikweni amanenaso chimodzimodzi. Onse awiri amaika mau awiri omwe mulibe. Ndinaphunzira chigiriki ndili ndi zaka 10 zakubadwa, ndi otsimikidzika muzowe ndikuyankhula. amaika mu mau' lamulo' kawiri. Lamulo. Paulo sayankhula choncho. iye amati:
Chocho mwa pangano la lamulo palibe thupi lomwe lidzapulumutsidwe, pakuti mwa lamulo ndi nzeru ya uchimo
Mumanena chabwino kodi cholinga cha lamulo chinali chani? cholinga cha lamulo anali mulungu kufuna kuonetsera vuto lomwe ulinalo, kuonetsera kuti ulindi vuto lomwe ndi tchimo. Lamulo litha kuonetsera vuto lako koma silingathane nalo. Litha kuthetsedwa mwa chisomo. mukusowekera lamulo kuti likutengereni kumalo komwe mukuona kuti mukusowekera chisomo, ichi ndicho cholinga chake.
Yakobo akufotokoza mu chaputara 2: 10-11 ya kalata yake
“Pakuti aliyense amene asunga lamulo lonse [tsopano akulankhula za lamulo la Mose] koma n’kulakwa pa chinthu chimodzi, ali wolakwa pa zonse. Pakuti Iye amene anati usachite chigololo ananenanso usaphe. Tsopano, ngati sunachite chigololo koma wapha, wakhala wophwanya lamulo.”
Mukuona zimene Yakobo akunena? Muyenera kusunga malamulo onse kapena simusunga malamulo. Kusunga malamulo makumi asanu ndi anayi ndi zisanu ndi zinayi pa zana sikutanthauza kusunga malamulo. Malamulo ndi dongosolo limodzi lonse.
Code: MV-4163-100-NYA
